Numbers 28:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aperekenso tonde kuti akhale nsembe yopepesera machimo, yopereka kwa Chauta. Aipereke kuwonjezera pa nsembe zopsereza ndi zopereka za zakumwa za tsiku ndi tsiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yaucimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yothira.