Numbers 28:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muperekenso chopereka cha chakudya wosakaniza ndi mafuta. Ufa wake ukhale wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yao ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yao ya ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo;