Numbers 28:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Chauta, pa tsiku la chikondwerero cha masabata, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'madyerero anu a masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena.