Numbers 28:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe aŵiri amphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya pfungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi;