Numbers 28:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanawankhosa wina uja muzimpereka madzulo, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa zonga zam'maŵa zija. Imeneyi ikhalenso nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mwana wa nkhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yace, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya pfungo lokoma la Yehova.