Numbers 28:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku la Sabata muzipereka anaankhosa aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema. Muziperekanso makilogaramu aŵiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka cha chakudya, ndipo muziperekanso chopereka cha chakumwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dzuwa la Sabata ana a nkhosa awiri a caka cimodzi, opanda cirema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yace yothira;