Numbers 29:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo muchite chikondwerero cholemekeza Chauta masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena, koma muchitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa tsiku la mwezi wachisanu ndi chiwiri, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. Muzichita madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamacita nchito ya masiku ena, koma mucitire Yehova madyerero masiku asanu ndi awiri;