Numbers 29:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku loyamba mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe khumi ndi atatu amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi. Nyama zonsezo zikhale zopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai, a chaka chimodzi, akhale opanda chilema;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipereka nsembe yotentha pa moto, kuti izikhala fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu, nkhosa zazimuna ziwiri, ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mubwere nayo nsembe yopsereza, ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe zamphongo khumi ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, akhale opanda cirema;