Numbers 29:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muperekenso choperaka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongo iliyonse,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yake yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a efa wa ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwana wangʼombe aliyense mwa ana angʼombe aamuna khumi ndi atatu aja, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Pa nkhosa iliyonse mwa nkhosa ziwiri zija, mukonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yace yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;