Numbers 29:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa tsiku lachiŵiri mupereke anaang'ombe khumi ndi aŵiri amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lachiwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, anaankhosa khumi ndi anai a chaka chimodzi, opanda chilema;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa tsiku lachiwiri muzipereka ana angʼombe aamuna khumi ndi awiri aja, nkhosa zazimuna ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi anayi a chaka chimodzi aja, zonse zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku laciwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai a caka cimodzi, opanda cirema;