Numbers 29:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, malinga ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka zopereka za chakudya ndi za chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;