Numbers 29:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muperekenso chopereka cha zakudya ndi zachakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za anaankhosa, monga mwa kuwerenga kwake, ndi kutsata lemba lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa, muzipereka chopereka cha chakudya ndi chakumwa molingana ndi chiwerengero cha nyamazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;