Numbers 29:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri, a chaka chimodzi, opanda chilema;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipereka chopereka chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Yehova, nsembe yopsereza ya ngʼombe imodzi yayimuna, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa amuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, zonse zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri, a caka cimodzi, opanda cirema;

Recommended Reading