Numbers 29:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mupereke zonsezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza yopereka mwezi ukakhala, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi nsembe zaufa ndi zopereka za chakumwa, potsata malamulo ake, kuti zitulutse fungo lokoma, nsembe zotentha pa moto, zopereka kwa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe zake zothira, monga mwa lemba lake, zikhale za fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi ndi zowonjezera pa nsembe zopsereza za mwezi ndi mwezi komanso za tsiku ndi tsiku pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi zopereka za chakumwa potsata malamulo ake. Izi ndi zopereka zotentha pa moto, zoperekedwa kwa Yehova, fungo lokoma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamodzi ndi nsembe yopsereza ya pamwezi, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, monga mwa lemba lace, zikhale za pfungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova.