Numbers 29:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma mupereke kwa Chauta nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma. Ikhale ya mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi. Musankhule nyama zopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya fungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma lokondweretsa Yehovayo; ngʼombe yayimuna imodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi. Zimenezi zizikhala zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mubwere nayo nsembe yopsereza kwa Yehova, ya pfungo lokoma; ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri a caka cimodzi; akhale kwa inu opanda cirema;