Numbers 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pakati pa Aisraele, ndaŵapatula Alevi, m'malo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa, amene amatsekula mimba ya mai wake. Aleviwo ndi anga,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwachotsa pakati pa ana a Israele m'malo mwa ana oyamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israele; ndipo Aleviwo ndi anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli m'malo mwa ana ovamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israyeli; ndipo Aleviwo ndi anga.