Numbers 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti ana onse aamuna oyamba kubadwa ndi anga. Pa tsiku lija lomwe ndidapha ana onse aamuna oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, ndidadzipatulira ana onse oyamba kubadwa a m'dziko la Israele, ana a anthu ndi a nyama omwe. Onsewo ndi anga, Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Ejipito ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israele, kuyambira munthu kufikira choweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israyeli, kuyambira munthu kufikira coweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.