Numbers 3:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo munthu amene anali mutu wa mabanja a Merari anali Zuriyele mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga zithando zao kumpoto kwa chihema cha Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya Kachisi ya kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleri wa magulu a mabanja a Amerari anali Zuriyeli mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga misasa yawo kumpoto kwa Chihema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.