Numbers 3:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene ankamanga zithando zao patsogolo pa chihema cha Mulungu kuvuma kotulukira dzuŵa, kutsogolo kwa chihema chamsonkhano, anali Mose ndi Aroni pamodzi ndi ana ake a Aroni. Iwoŵa adaŵapatsa udindo wosamala kayendetsedwe ka chipembedzo m'malo opatulika, zonse zimene ankayenera kuchita m'malo mwa Aisraele. Munthu wina aliyense wofika pafupi ankayenera kuphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose ndi Aaroni ndi ana ake aamuna ankamanga misasa yawo kummawa kwa chihema, kuyangʼana kotulukira dzuwa, kutsogolo kwa tenti ya msonkhano. Anali ndi ntchito yosamalira malo wopatulika mʼmalo mwa Aisraeli. Aliyense woyandikira malo wopatulika ankayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la kacisi, kum'mawa, pa khomo la cihema cokomanako koturukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ace amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israyeli; koma mlendo wakuyandikizako amuphe,