Numbers 3:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi onse amene Mose pamodzi ndi Aroni adaŵerenga potsata mabanja ao, Chauta ataŵalamula kutero, ndiye kuti amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, anali 22,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi onse amene Mose ndi Aaroni anawawerenga potsatira lamulo la Yehova monga mwa magulu a mabanja awo, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kapena kupitirirapo anali 22,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.