Numbers 30:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pa tsiku limene mwamuna wake wamva zimenezo, akamletsa mkaziyo kuti asachite zimene adalumbirazo, palibe lamulo lomkakamiza mkaziyo kuchita zimene adalumbira kapenanso zimene adalonjeza. Mwamuna wake waletsa, ndipo Chauta adzamkhululukira mkaziyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati mwamuna wake anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zotuluka m'milomo yake kunena za zowinda zake, kapena za chodziletsa cha moyo wake sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati mwamuna wace anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zoturuka m'milomo yace kunena za zowinda zace, kapena za codziletsa ca moyo wace sizidzakhazikika; mwamuna wace anazifafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira Iye.