Numbers 30:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwamuna wake ali ndi mphamvu za kuvomereza kapena kukana zimene mkaziyo adalumbira kapena zimene adalonjeza zokhudza za kudzilanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chowinda chilichonse, ndi cholumbira chilichonse chodziletsa chakuchepetsa nacho moyo, mwamuna wake achikhazikira, kapena mwamuna wake achifafaniza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cowinda ciri conse, ndi columbira ciri conse codziletsa cakucepetsa naco moyo, mwamuna wace acikhazikira, kapena mwamuna wace acifafaniza.