Numbers 30:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati m'maŵa mwake ndi masiku otsatirawo mwamuna wake samkaniza, atamva zimenezo, mkaziyo achitedi zonse zimene adalumbira, kapena zimene adalonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa choti sadamuuze kanthu mkaziyo pa tsiku limene adamva.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwamuna wake akhala naye chete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zake zonse, kapena zodziletsa zake zonse, zili pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye chete tsikuli anazimva iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mwamuna wace akakhala naye cete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zace zonse, kapena zodziletsa zace zonse, ziri pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye cete tsikuli anazimva iye.