Numbers 30:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo malamulo amene Chauta adalamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso za bambo ndi mwana wake wamkazi amene akadali mtsikana wokhalabe m'nyumba ya bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, pakati pa atate ndi mwana wake wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wace, pakati pa atate ndi mwana wace wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wace.