Numbers 30:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pamene munthu wamwamuna alumbira kwa Chauta kapena alonjeza kuti adzachitadi zimene walumbira, asaphwanye lonjezo lakelo. Achite molingana ndi zimene adalumbira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akacitira Yehovacowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wace codziletsa, asaipse mau ace; azicita monga mwa zonse zoturuka m'kamwa mwace.