Numbers 30:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
tsono bambo wake nkumva za kulumbira kwakeko ndi za malonjezo amene walumbira kuti adzachitadi, koma bambo wakeyo osalankhula kanthu, mwanayo achitedi zimene adalumbirazo. Ayenera kuchitadi zonse zimene walonjezazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo atate wake akamva chowinda chake, ndi chodziletsa chake anamanga moyo wake nacho, koma wakhala naye chete atate wake; pamenepo zowinda zake zonse zidzakhazikika, ndi chodziletsa chilichonse wamanga nacho moyo wake chidzakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo atate wace akamva cowinda cace, ndi codziletsa cace anamanga moyo wace naco, koma wakhala naye cete atate wace; pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi codziletsa ciri: conse wamanga naco moyo wace cidzakhazikika.