Numbers 30:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma bambo wake akamkaniza mwanayo pa tsiku lomwe wamva zimenezo, palibe lamulo lomkakamiza mwanayo kuti achite zimene adalumbirazo ndi zimene adalonjezazo. Chauta adzamkhululukira mwanayo chifukwa choti bambo wake adamkaniza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma atate wake akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zake zonse, ndi zodziletsa zake zonse anamanga nazo moyo wake, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wake anamletsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma atate wace akamletsa tsiku lakumva iye; zowinda zace zonse, ndi zodziletsa zace zonse anamanga nazo moyo wace, sizidzakhazikika; ndipo Yehova adzamkhululukira, popeza atate wace anamletsa.