Numbers 30:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
tsono mwamuna wake nkumva, koma osamuuza kanthu mkaziyo pa tsiku lomwe wamvalo, mkaziyo achitedi zimene walumbirazo, achite ndithu zimene walonjezazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nakazimva mwamuna wake, nakakhala naye chete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zake zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wake zidzakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nakazimva mwamuna wace, nakakhala naye cete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zace zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.