Numbers 30:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati pa tsiku limene mwamunayo wamva zimenezo, amkaniza, pamenepo ammasula mkaziyo kwa zimene adalumbira ndi kwa zimene adalankhula mosaganiza bwino, ndipo Chauta adzamkhululukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mwamuna wake akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza chowinda chake anali nacho, ndi zonena zopanda pake za milomo yake, zimene anamanga nazo moyo wake; ndipo Yehova adzamkhululukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kama mwamuna wace akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza cowinda cace anali naco, ndi zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace; ndipo Yehova adzamkhululukira.