Numbers 31:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja akazi ameneŵa adatsata uphungu wa Balamu, nasokeretsa Aisraele kuti asachitenso zokhulupirika pamaso pa Chauta ku Peori kuja, kotero kuti mliri udagwera mpingo wa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, awa analakwitsa ana a Israele pa Yehova ndi cha Peori chija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, awa analakwitsa ana a Israyeli pa Yehova nilica Peoricija, monga adawapangira Balamu; kotero kuti kunali mliri m'khamu la Yehova.