Numbers 31:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pa gawo la Aisraele, mtengeko chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, pa anthu, ng'ombe, abulu, nkhosa ndi pa nyama zonse zoŵeta, ndipo mupatse Alevi amene amayang'anira Chihema cha Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ku gawo la ana a Israyeli utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa aburu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova.