Numbers 31:47 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa gawo la Aisraelelo, Mose adatengako chofunkha chimodzi pa zofunkha makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo adapatsa Alevi amene ankayang'anira Chihema cha Chauta, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa Kachisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwa gawolo la ana a Israyeli Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa kacisi wa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.