Numbers 31:50 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tabwera naco copereka ca Yehova, yense cimene anacipeza, zokometsera zagolidi, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kucita cotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova.