Numbers 31:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adaŵatumiza ku nkhondo anthuwo, chikwi chimodzi pa fuko lililonse, pamodzi ndi Finehasi mwana wa wansembe Eleazara, iyeyu atanyamula zipangizo za ku malo opatulika ndi malipenga ochenjeza m'manja mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.