Numbers 32:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali ndi ng'ombe zambiri. Adaona dziko la Yazere ndi dziko la Giliyadi kuti linali ndi malo oyenera kuŵeterako ng'ombe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ana a Rubeni ndi ana Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazere, ndi dziko la Giliyadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ana a Rubeni ndi ana a Gadi anali nazo zoweta zambirimbiri; ndipo anapenyerera dziko la Yazeri, ndi dziko la Gileadi, ndipo taonani, malowo ndiwo malo a zoweta.