Numbers 32:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Ndithudi palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu otuluka m'dziko la Ejipito, kuyambira wa zaka makumi aŵiri ndi wopitirirapo, amene adzaone dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, chifukwa sadanditsate kwathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu adakwerawo kutuluka m'Ejipito, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo; popeza sananditsate Ine ndi mtima wonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu adakwerawo kuturuka m'Aigupto, kuyambira wa zaka makumi awiri ndi mphambu sadzaona dziko limene ndinalumbirira Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo; popeza sananditsata Ine ndi mtima wonse;