Numbers 32:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwo adasendera kwa Mose namuuza kuti, “Poyamba mutilole kuti timange kuno makola a nkhosa zathu, ndi mizinda yoti ana athu azikhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayandikiza, nati Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayandikiza, nati, Tidzamangira zoweta zathu makola kuno, ndi ana athu midzi; koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israyeli, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao;