Numbers 32:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake tidzatenga zida zankhondo ndi kutsogolera Aisraele mpaka titakaŵafikitsa ku malo ao. Koma ana athu adzakhala m'mizinda yamalinga, chifukwa choopa anthu a m'dziko muno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ife tidzakhala okonzeka ndi kufulumira pamaso pa ana a Israele, kufikira tidawafikitsa kumalo kwao; ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga chifukwa cha okhala m'dzikomo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ang'ono athu adzakhala m'midzi ya malinga cifukwa ca okhala m'dzikomo.