Numbers 32:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mpaka kugonjetsa dzikolo pamaso pa Chauta. Mukatero, pambuyo pake mudzabwerera kuno, chifukwa mudzakhala mutagwirira ntchito Chauta ndi Aisraele. Pamenepo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osachimwira Yehova ndi Israele; ndipo dziko ili lidzakhala lanulanu pamaso pa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osacimwira Yehova ndi Israyeli; ndipo dziko ili lidzakhala lanu lanu pamaso pa Yehova.