Numbers 32:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati ana a Gadi ndi a Rubeni onse amene angathe kutenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Chauta. Adzaoloka nanu mtsinje wa Yordani, nadzagonjetsa dziko lili patsogolo panulo, mudzaŵapatse dziko la Giliyadi kuti likhale lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordani, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Giliyadi likhale laolao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordano, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Gileadi likhale lao lao;