Numbers 32:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo Mose adapatsa ana a Gadi ndi a Rubeni ndiponso theka la fuko la Manase, mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dziko lonse pamodzi ndi mizinda ndi milaga yake, ndiye kuti mizinda yonse ya m'dziko lonselo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi fuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani, dzikoli ndi midzi yake m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anawapatsa, ndiwo ana a Gadi, ndi ana a Rubeni ndi pfuko la hafu la Manase mwana wa Yosefe, dziko la Sihoni mfumu ya Aamori, ndi dziko la Ogi mfumu ya Basana, dzikoli ndi midzi yace m'malire mwao, ndiyo midzi ya dziko lozungulirako,