Numbers 33:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanyamuka ku Ramsesi pa mwezi woyamba, pa tsiku la 15 la mweziwo. M'maŵa mwake, litapita tsiku la Paska, Aisraele adatuluka m'dziko la Ejipito mokondwa, anthu onse a ku Ejipito akupenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,