Numbers 33:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta atamlamula, wansembe Aroni adakwera phiri la Hori nakafera komweko, chaka cha 40 Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto zaka makumi anai, mwezi wacisanu, tsiku loyamba la mwezi.