Numbers 33:54 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzalandira dzikolo kuti likhale choloŵa chanu mwamaere, potsata mabanja anu. Fuko lalikulu lilandire choloŵa chachikulu, ndipo fuko laling'ono lilandire choloŵa chaching'ono. Dziko lililonse limene maere agwere munthu, likhale lake la munthuyo. Mudzalandire choloŵa chanu potsata mafuko a makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.