Numbers 33:55 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mukapanda kupirikitsa nzika zam'dzikomo pamene mukufika, amene mwaŵalola kuti atsalirewo adzakhala ngati zisonga zokubayani m'maso, ndiponso ngati minga m'mbali mwanu, ndipo adzakuvutani m'dziko m'mene mukakhalemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mukapanda kupitikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakubvutani m'dziko limene mukhalamo.