Numbers 34:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafuko aŵiriwo ndi thekalo adalandira kale choloŵa chao patsidya pa mtsinje wa Yordani ku Yeriko chakuvuma kotulukira dzuŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mafuko awiriwa ndi hafu adalandira cholowa chao tsidya lija la Yordani ku Yeriko, kum'mawa, kotulukira dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mapfuko awiriwa ndi hafu adalandira colowa cao tsidya lija la Yordano ku Yeriko, kum'mawa, koturukira dzuwa.