Numbers 35:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mupatule mizinda ina kuti ikhale mizinda yanu yothaŵirako, kumene munthu wopha mnzake mwangozi azithaŵirako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzake wosati dala athawireko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
sankhani midzi ina kuti ikhale mizinda yanu yopulumukirako, kumene munthu wopha munthu wina mwangozi angathawireko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
muikire midzi ikukhalireni midzi yopulumukirako; kuti wakupha mnzace wosati dala athawireko.