Numbers 35:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizindayo idzakhala malo obisalamo pothaŵa munthu wofuna kubwezera choipa, kuti munthu wopha mnzake mwangoziyo asaphedwe, mpaka akaime pamaso pa mpingo kuti umuweruze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzakhala malo obisalako pothawa munthu wofuna kulipsira, kuti munthu wopha mnzake mwangozi asaphedwe mpaka akayime pamaso pa gulu la anthu kuti akaweruzidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo midziyo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzace asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.