Numbers 35:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizinda isanu ndi umodziyo idzakhala yothaŵirako Aisraele, alendo ndi anthu okhala pakati pao, kuti wina aliyense wopha munthu mnzake mwangozi azithaŵirako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israele, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti aliyense adamupha munthu osati dala athawireko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Midzi isanu ndi umodzi idzakhala malo opulumukirako Aisraeli, alendo ndi anthu ena onse okhala pakati pawo kuti wina aliyense wopha mnzake mwangozi adzathawireko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Midzi isanu ndi umodzi imene ndiyo yopulumukirako ana a Israyeli, ndi mlendo, ndi wokhala pakati pao; kuti ali yense adamupha munthu osati dala athawireko.