Numbers 35:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati munthu amenya mnzake ndi mwala, mwala wake woti nkupha munthu, mnzakeyo nafadi, ndiye kuti ndi wopha munthu ameneyo. Tsono wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kapenanso ngati wina wake ali ndi mwala mʼdzanja mwake womwe ungaphe munthu, ndipo agenda nawo wina, munthu winayo nʼkufa, ndiye kuti iyeyo ndi wakupha ndipo wakuphayo adzayenera kuphedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kapena akamkantha m'dzanja muli mwala, wakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.